Solar Power Station, Salima.
Magetsi ayatsidwa lero! President wathu anawonetstetsa kuti ntchito yomwe inabweletsedwa mu dziko lino ndi President Joyce Banda komanso kuyambidwa pansi pa President Peter Mutharika imalizidwe mwa makono ndiponso mosasolora olo one Tambala. Ndithu kuyambira chaka chino, national grid yathu yawonjezedwa ndi 60 Megawatts ndipo zoti magetsi amathima mwachisawawa zikhala mbiri yakale.Kumanyadira dziko lanu, aMalawi. Zotelezitu mulibe mmayiko ambiri ndipo power station imeneyi ndi imodzi mwa zazikulu kwambiri mu Africa ndipo si yokhayitu kwathu kuno; nakonso ku Golomoti uko ilipo yina. Kwanteretu chidzuwa chathuchi tachipezera ntchito ndipo tonse tipindura pogwilitsa magetsi osawononga chilengedwe. Pa ground padziwala ngati masana koma uli usiku!
Leave a Reply